Nduna yoona za m'dziko a Ken Zikhale Ng'oma yati makina amene akuwagwiritsa ntchito posindikiza ziphaso zoyendera (passports) akugwira ntchitoyo mochedwa kwambiri. Ndunayi yati makinawa akumasindikiza ziphaso zosadutsa 500 patsiku zimene zikuchititsa ntchitoyi kumagwirika mochedwa. Iwo ati pakadali pano nthambiyi ili ndi ziphaso zofuna kusindikiza zokwana 35,000 zimene ikudikira koma apereka chikhulupiriro kuti izi zitheka posachedwapa. […]
The post Vuto la ma pasipoti lizatha? A Zikhale akuti makina alipowo akuchedwa, akupanga mapasipoti 500 okha pa tsiku appeared first on Malawi Nyasa Times - News from Malawi about Malawi.